Skip to content
BibleKenya

Maluko

Mark

Introduction from this edition

Uthenga Wabwino ngati umo udalembedwela ni

Maluko

Yayo yalimo mchikalakala ichi

Uthenga Wabwino ngati umo udaledwela ni Maluko, ni chimojhi cha vikalakala vinayi pa chipangano cha chipano icho chikambilila umoyo wa Yesu Kilisito. Kila chimojhi chake avitana vikalakala ivi Injili mate yake, “Uthenga Wabwino.” Vikalakala ivi Vidalembedwa yapo Yesu wadathomwalila, vidalembedwa ni Mathayo, Maluko, Luka ni Yohana. Uthenga Wabwino udalembedwa ni Maluko ni wochepa pa vikalakala ivi vonje vinayi. Chimchijha ikhulupilika kuti chikalakala ichi chidali choyamba kulembwedwa pa vikalakala vonjhe, mchaka cha 65 mbaka 70 yapo Yesu wadathobadwa. Osoma ambili akhulupilila kuti chikalakala ichi chidalembedwa yapo wadali ku Loma, ndande ya kwathila mtima a Kilisito adali ku Loma.

Chimchijha uyu Maluko wadajhiwika ngati Yohana Maluko. Wadali ochatila wa Mtumwi Paulo, ni Banaba, nambho sifa yake idadechedwa yapo wadasiya ulendo wao munjhito yao wa utumwi. Machitidwe ya atumwi 13:13. Pambuyo Maluko wadapangajho ulendo, ni Banaba. Machitidwe ya atumwi 15:37-39. Maluko wadajhiwikanjho, ngati bwenji wa pafupi wa Petulo. Petulo woyamba 5:13. Nambho Maluko wadali osati mmojhi wa amboni adamuona Yesu kwa maso yao. Osoma ambili akhulupilila kuti Maluko wadalemba nghani zambili kuchokela mchikalakala cha Petulo, ni umenewo nde msingi wa Uthenga Wabwino uwo udalembedwa ni Maluko. Mkati mwa uthenga uwu Maluko wakambilila utumwi ni mayaluzo ya Yesu.

Yayo yali muchikalakala ichi

Maluko wachijhiwicha chikalakala mu Maluko 1:1-13.

Maluko wafotokoza njhito ya Yesu yapo wadali ku Galilaya mu Maluko 1:14, 8:21.

Maluko wafotokoza ulendo wa Yesu wopita ku Yelusalemu mu Maluko 8:22, 10:52.

Maluko wamalizila kwa kulemba ndhawi iyo Yesu yapo wadali ku Yelusalemu, pamojhi ni nyifa yake, ni kuhyuka kwake, ni wandhu akamba mthila mu Maluko 11:1, 16:8.

Nyanja Tanzania Bible Version. Copyright © The Word for the World International. Licensed under CC BY-SA 4.0. Source: Open.Bible. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-11-09.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.