Skip to content
BibleKenya

Agalatiya

Galatians

Introduction from this edition

Kalata ya Poolo kwa

Agalatiya

Uchogolole

Kalata ya Agalatiya idalembedwa ni Mtumwi Poolo munghope ya 1:1. Iyi ni kalata iyo wadalemba poolo kwa wandhu adamkhulupilila Yesu yawo adali ku mujhi wa Galatiya pakati pa chaka cha 48 ni 57 pambuyo po badwa Kilisito. Ikhozekana Agalatiya amakhala kumujhi wa Galatiya mujhi uwo umalamulidwa ni Aloma. Osoma abibiliya sajhiwa uko wadalipo poolo yapo wamalemba kalata iyi, nambho ambili aganiza kuti wadalemba yapo wadali kumujhi wa Efeso kapina kumujhi Kolitho.

Poolo wadalemba kalata ino ndande ya wandhu wonjhe yawo adamkhulupilila Kilisito yawo adali kumujhi wa Galatiya yani wajha adali Ayahudi ni wajha adali osati Ayahudi. Wadalemba kalata ino ndande ya kuyachucha mayaluzo ya mthila yayo yamafuna Akilisito achate thauko la chiyahudi izo zili mu chipangano cha kale hasa yaluzo la kuchitidwa mdulidwe. Padali ni gulu la wandhu pa gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito, adajhitana Ayuda, anyiiwo adakakamiza wandhu yawo adamkhulupilila Yesu yawo adali osati Ayahudi kuti achitidwe mdulidwe. Chimchijha wandhu ameneo amafunjha mafunjho kuti yani wampacha Poolo lamulo lochita njhito imeneyo. Poolo wadateteza utumwi wake kwa kufotokozela nghani zake zina mughope ya 1:11 mbaka nghope ya 2:14 ni wadateteza Uthenga Wabwino wadafotokoza kuti uwomboli ukhoza kupezeka kwa kumkhulupilila Yesu Kilisito munghope ya 2:16. Machokelo ya chikondi cha Mnungu waulangiza kwa wandhu, ni uomboli siukhulupila vichito va wandhu.

Yayo yalimo mukalata iyi

Poolo wayamba kalata yake kwa kwaalonjela wandhu adamkhulupilila Yesu ku Galatiya munghope yo 1:1-5.

Ndiipo poolo wafotokozela nghani za ukhalo wake kwa pang'ono, dala wateteze kuvomelezeka kwake pa kuyaluza, ni kuchimikiza kuti wadayesa kukhala kwa kuchata thauko, nambho thauko silidamthangatile munghope ya 1:6 mbaka nghope ya 2:21.

Pambuyo wafotokozela kupunda njhito ya Thauko ni Ubwino pa uwomboli munghope ya 3 mbaka nghope ya 4.

Ndiipo wafotokozela maagizo yina ya pamojhi kulangiza umo ifunikila Akilisito kukhala bwino munghope ya 5 mbaka nghope ya 6:10.

Poolo wamalizila kalata yake kwa kuchocha moni ni pembho lothela uku ni wakumbucha kuti kung'anamulidwa ni Mnungu ni kuchitidwa mundhu wachipano ni kufunika kupunda kusiyana ni thauko ni vindhu va kubwalo ngati kuchitidwa mduludwe munghope ya 6:11-18.

Nyanja Tanzania Bible Version. Copyright © The Word for the World International. Licensed under CC BY-SA 4.0. Source: Open.Bible. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-11-09.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.