Skip to content
BibleKenya

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Nehemiya 7

Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”

Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo

Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.

Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:

Zidzukulu za Parosi

2,172

Zidzukulu za Sefatiya

372

Zidzukulu za Ara

652

Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu)

2,818

Zidzukulu za Elamu

1,254

Zidzukulu za Zatu

845

Zidzukulu za Zakai

760

Zidzukulu za Binuyi

648

Zidzukulu za Bebai

628

Zidzukulu za Azigadi

2,322

Zidzukulu za Adonikamu

667

Zidzukulu za Abigivai

2,067

Zidzukulu za Adini

655

Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)

98

Zidzukulu za Hasumu

328

Zidzukulu za Bezayi

324

Zidzukulu za Harifu

112

Zidzukulu za Gibiyoni

95.

Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa

188

Anthu a ku Anatoti

128

Anthu a ku Beti-Azimaveti

42

Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti

743

Anthu a ku Rama ndi Geba

621

Anthu a ku Mikimasi

122

Anthu a ku Beteli ndi Ai

123

Anthu a ku Nebo winayo

52

Ana a Elamu wina

1,254

Zidzukulu za Harimu

320

Zidzukulu za Yeriko

345

Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono

721

Zidzukulu za Senaya

3,930.

Ansembe anali awa:

A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa)

973

Zidzukulu za Imeri

1,052

Zidzukulu za Pasi-Huri

1,247

Zidzukulu za Harimu

1,017.

Alevi anali awa:

A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya

74.

Anthu oyimba:

Zidzukulu za Asafu

148.

Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za

Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai

138.

Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za

Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,

Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni

Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,

Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,

Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,

Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,

Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,

Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,

Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,

Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema

Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.

Zidzukulu za antchito a Solomoni:

Zidzukulu za

Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida

zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,

zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu

zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.

Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo

392.

Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.

Zidzukulu za

Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda

642.

Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:

zidzukulu za

Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).

Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.

Ezara Awerenga Malamulo

Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero. Copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Licensed under CC BY-SA 4.0.   “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Source: eBible.org. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-10-25.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.