Skip to content
BibleKenya

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 35

Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti,

“Kodi mukuganiza kuti mukukhoza?

Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’

Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani,

ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’

“Ine ndikufuna ndikuyankheni inu

pamodzi ndi abwenzi anu omwe.

Yangʼanani kumwamba ndipo muone

mitambo imene ili kutali ndi inuyo.

Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani?

Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye?

Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani?

Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu?

Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo,

ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.

“Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa;

akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu.

Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga,

amene amatisangalatsa nthawi ya usiku,

amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi

ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’

Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye

chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa.

Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake;

Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.

Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti

Iye saona zimene zikuchitika.

Iye adzaweruza molungama ngati

inu mutamudikira

ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango,

zoyipa zambiri zimene anthu amachita,

abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake,

mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero. Copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Licensed under CC BY-SA 4.0.   “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Source: eBible.org. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-10-25.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.