Skip to content
BibleKenya

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 18

Mawu a Bilidadi

Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

“Kodi iwe Yobu utsiriza liti zoyankhula zakozi?

Khala munthu wozindikira zinthu ndipo ukatero ife tidzayankhula.

Chifukwa chiyani ukutiyesa ngati ngʼombe

ndi kuoneka ngati opusa mʼmaso mwako?

Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako,

kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo?

Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake?

“Nyale ya munthu woyipa yazimitsidwa;

malawi a moto wake sakuwalanso.

Kuwala kwa mʼnyumba mwake kwasanduka mdima;

nyale ya pambali pake yazima.

Mayendedwe ake amgugu azilala;

fundo zake zomwe zamugwetsa.

Mapazi ake amulowetsa mu ukonde

ndipo akungoyendayenda mu ukondewo.

Msampha wamkola mwendo;

khwekhwe lamugwiritsitsa.

Amutchera msampha pansi mobisika;

atchera diwa pa njira yake.

Zoopsa zikumuchititsa mantha kumbali zonse,

zikutsatira mayendedwe ake onse.

Mphamvu zake zatha chifukwa cha njala,

tsoka likumudikira.

Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse;

miyendo yake, manja ake, zonse zawola.

Wachotsedwa mʼnyumba imene ankadalira,

ndipo amukokera ku imfa, mfumu ya zoopsa zonse.

Mʼnyumba mwake zonse zachotsedwamo;

awazamo sulufule kuti aphe tizirombo ta matenda.

Mizu yake ikuwuma pansi

ndipo nthambi zake zikufota

Sadzakumbukiridwanso pa dziko lapansi;

sadzakhalanso ndi chinthu chomutchukitsa mʼdziko.

Amuchotsa pa malo owala ndi kumuponya ku mdima,

ndipo amupirikitsa pa dziko lonse.

Iye alibe ana kapena zidzukulu pakati pa anthu ake,

kulibe wotsala kumene iye ankakhala.

Anthu akumadzulo adabwa kwambiri ndi tsoka lake;

anthu akummawa agwidwa ndi mantha aakulu.

Ndithudi, izi ndiye zimagwera munthu woyipa;

amenewa ndiye mathero a munthu amene sadziwa Mulungu.”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero. Copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Licensed under CC BY-SA 4.0.   “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Source: eBible.org. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-10-25.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.