Skip to content
BibleKenya

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 11

Mawu a Zofari

Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti,

“Kodi mawu ambirimbiriwa nʼkukhala osayankhidwa?

Kodi munthu woyankhulayankhulayu nʼkulungamitsidwa?

Kodi anthu nʼkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku?

Kodi palibe wina amene adzakudzudzule pamene ukuyankhula zonyoza?

Iwe ukunena kwa Mulungu kuti, ‘Zikhulupiriro zanga ndi zopanda zolakwika

ndipo ndine wangwiro pamaso panu.’

Aa, nʼkanakonda Mulungu akanayankhula

kuti Iye atsekule pakamwa pake kutsutsana nawe

ndi kukuwululira chinsinsi cha nzeru yake,

pakuti nzeru yeniyeni ili ndi mbali ziwiri.

Dziwa izi: Mulungu wayiwala machimo ako ena.

“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu?

Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?

Zili kutali kupambana mayiko akumwamba, nanga ungachite chiyani?

Ndi zakuya kupambana kuya kwa manda, nanga ungadziwe chiyani?

Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana dziko lapansi

ndipo ndi wopingasa kupambana nyanja.

“Ngati Iye atabwera ndi kukutsekera mʼndende

nakutengera ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa?

Ndithudi, Mulungu amazindikira anthu achinyengo;

akaona choyipa, kodi sachizindikira?

Munthu wopanda nzeru sizingatheke kukhala wanzeru

monganso mwana wa bulu wakuthengo sangasanduke munthu.

“Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye

ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo,

ngati utaya tchimo limene lili mʼdzanja lako

ndi kusalola choyipa kuti chikhale mʼmoyo mwako,

udzatukula mutu wako wosachita manyazi;

udzayima chilili ndipo sudzachita mantha.

Udzayiwala ndithu zowawa zako,

zidzakhala ngati madzi amene apita kale.

Moyo wako udzawala kupambana usana,

ndipo mdima udzakhala ngati mmawa.

Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo;

ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka.

Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza

ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo.

Koma anthu oyipa adzafuna thandizo osalipeza,

ndipo adzasowa njira yothawirapo;

chiyembekezo chawo chidzakhala imfa basi.”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero. Copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Licensed under CC BY-SA 4.0.   “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Source: eBible.org. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-10-25.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.