Skip to content
BibleKenya

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 12

Kudziyeretsa kwa Mkazi Atabala Mwana

Yehova anayankhula ndi Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera, nabala mwana wa mwamuna, mkaziyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, ngati pa masiku ake akusamba. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mwanayo achite mdulidwe. Mkaziyo adikire masiku ena 33 kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kalikonse koyera kapena kulowa mʼmalo wopatulika mpaka masiku a kuyeretsedwa kwake atatha. Ngati abala mwana wamkazi, adzakhala wodetsedwa kwa masabata awiri, monga zikhalira pa nthawi yake yosamba. Ndipo mkaziyo adikire masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda akewo.

“ ‘Masiku ake wodziyeretsa akatha, kaya ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la tenti ya msonkhano kuti ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi chiwunda cha nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Wansembeyo apereke zimenezi pamaso pa Yehova pochita mwambo wopepesera mkaziyo. Ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku msambo wake.

“ ‘Amenewa ndiwo malamulo a mkazi amene wabala mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ngati mkaziyo sangathe kupeza mwana wankhosa, abwere ndi njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri: imodzi ikhale ya nsembe yopsereza ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera wa mkaziyo ndipo adzayeretsedwa.’ ”

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero. Copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Licensed under CC BY-SA 4.0.   “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Source: eBible.org. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-10-25.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.