Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
Ezara 2
Mʼndandanda wa Ayuda amene Anabwerera
Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake. Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).
Chiwerengero cha anthu aamuna a Israeli chinali chotere:
Zidzukulu za Parosi
2,172
zidzukulu za Sefatiya
372
zidzukulu za Ara
775
zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu)
2,812
zidzukulu za Elamu
1,254
zidzukulu za Zatu
945
zidzukulu za Zakai
760
zidzukulu za Bani
642
zidzukulu za Bebai
623
zidzukulu za Azigadi
1,222
zidzukulu za Adonikamu
666
zidzukulu za Bigivai
2,056
zidzukulu za Adini
454
zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)
98
zidzukulu za Bezayi
323
zidzukulu za Yora
112
zidzukulu za Hasumu
223
zidzukulu za Gibari
95.
Anthu a ku Betelehemu
123
Anthu aamuna a ku Netofa
56
Anthu aamuna a ku Anatoti
128
Anthu aamuna a ku Azimaveti
42
Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti
743
Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba
621
Anthu aamuna a ku Mikimasi
122
Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai
223
Anthu aamuna a ku Nebo
52
Anthu aamuna a ku Magaibisi
156
Anthu aamuna a ku Elamu wina
1,254
Anthu aamuna a ku Harimu
320
Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono
725
Anthu aamuna a ku Yeriko
345
Anthu aamuna a ku Sena
3,630.
Ansembe anali awa:
Zidzukulu za Yedaya (kudzera mu banja la Yesuwa)
973
Zidzukulu za Imeri
1,052
Zidzukulu za Pasuri
1,247
Zidzukulu za Harimu
1,017.
Alevi anali awa:
Zidzukulu za Yesuwa ndi Kadimieli (kudzera mwa ana a Hodaviya)
74.
Anthu oyimba nyimbo anali awa:
Zidzukulu za Asafu
128.
Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za Salumu, zidzukulu za Ateri, zidzukulu za Talimoni, zidzukulu za Akubu, zidzukulu za Hatita ndi zidzukulu za Sobai
139.
Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Zidzukulu za
Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,
zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,
zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,
zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,
zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,
zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,
zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,
zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,
zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.
Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi:
Zidzukulu za
Sotai, zidzukulu za Hasofereti, zidzukulu za Peruda,
zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu,
zidzukulu za Pokereti, Hazebayimu ndi Ami.
Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali
392.
Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali
652.
Ndi ena pakati pa ansembe anali awa:
Zidzukulu za
Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)
Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo. Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.
Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360, kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200. Anali ndi akavalo 736, nyulu 245, ngamira 435 ndi abulu 6,720.
Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale. Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.
Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero. Copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Licensed under CC BY-SA 4.0. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Source: eBible.org. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.
Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-10-25.