Skip to content
BibleKenya

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 8

Musayiwale Yehova

Samalani potsata lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mukhale ndi moyo ndi kuchulukana kuti mulande ndi kulowa mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzapereka kwa makolo anu. Kumbukirani mmene Yehova Mulungu wanu anakutsogolerani njira yonse mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kukutsitsani ndi kukuyesani kuti adziwe chimene chinali mu mtima mwanu ngati mungathe kusunga malamulo ake kapena ayi. Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova. Mʼzaka makumi anayi zimenezi, zovala zanu sizinangʼambike ndipo mapazi anu sanatupe. Tsono dziwani mu mtima mwanu kuti monga abambo amalanga mwana wawo, momwemonso Yehova Mulungu wanu amakulangani.

Samalirani malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira yake ndi kumuopa Iye. Pakuti Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino, dziko lokhala ndi mitsinje ndi mathawale a madzi, akasupe oyenderera mu zigwa ndi mʼmapiri, dziko lokhala ndi tirigu ndi barele, mpesa ndi mitengo ya mkuyu, makangadza, mafuta a olivi ndi uchi; dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa.

Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani. Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo, ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka, mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo. Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma. Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino. Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.” Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.

Ine ndine mboni yokutsutsani lero lino, kuti mukayiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutsata milungu ina nʼkumayigwadira, mudzawonongeka ndithu. Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero. Copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Licensed under CC BY-SA 4.0.   “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Source: eBible.org. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-10-25.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.