Skip to content
BibleKenya

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 1

Mbiri ya Makolo Kuchokera pa Adamu Mpaka pa Abrahamu

Mpaka pa Ana a Nowa

Adamu, Seti, Enosi Kenani, Mahalaleli, Yaredi, Enoki, Metusela, Lameki, Nowa.

Ana a Nowa,

Semu, Hamu ndi Yafeti.

Fuko la Yafeti

Ana aamuna a Yafeti anali:

Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.

Ana aamuna a Gomeri anali:

Asikenazi, Rifati ndi Togarima

Ana aamuna a Yavani anali:

Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.

Fuko la Hamu

Ana aamuna a Hamu anali:

Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani

Ana aamuna a Kusi anali:

Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka

Ana aamuna a Raama anali:

Seba ndi Dedani.

Kusi anali abambo a Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu

kwambiri pa dziko lapansi.

Igupto ndiye kholo la

Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, Apaturusi, Akasilu (kumene kunachokera Afilisti) ndi Akafitori.

Kanaani anabereka mwana wake wachisamba Sidoni,

ndipo anaberekanso Ahiti, Ayebusi, Aamori, Agirigasi Ahivi, Aariki, Asini Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.

Fuko la Semu

Ana aamuna a Semu anali:

Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.

Ana aamuna a Aramu anali:

Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.

Aripakisadi anabereka Sela

ndipo Selayo anabereka Eberi:

Eberi anabereka ana aamuna awiri:

wina anamutcha Pelegi, chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.

Yokitani anabereka

Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, Hadoramu, Uzali, Dikila Obali, Abimaeli, Seba, Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.

Semu, Aripakisadi, Sela

Eberi, Pelegi, Reu

Serugi, Nahori, Tera

ndi Abramu (amene ndi Abrahamu).

Banja la Abrahamu

Ana a Abrahamu ndi awa:

Isake ndi Ismaeli.

Zidzukulu za Hagara

Zidzukulu zake zinali izi:

Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli, kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Awa anali ana a Ismaeli.

Zidzukulu za Ketura

Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu anali awa:

Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa.

Ana a Yokisani ndi awa:

Seba ndi Dedani

Ana aamuna a Midiyani anali,

Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.

Onsewa anali zidzukulu za Ketura.

Zidzukulu za Sara

Abrahamu anabereka Isake.

Ana a Isake anali awa:

Esau ndi Israeli.

Ana a Esau

Ana aamuna a Esau anali awa:

Elifazi, Reueli, Yeusi, Yolamu ndi Kora.

Ana a Elifazi anali awa:

Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi:

Amene anabereka ndi Timna: Amaleki.

Ana a Reueli anali awa:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza.

Anthu a ku Seiri ku Edomu

Ana a Seiri anali awa:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani.

Ana aamuna a Lotani anali awa:

Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.

Ana aamuna a Sobala anali awa:

Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.

Ana aamuna a Zibeoni anali awa:

Ayiwa ndi Ana.

Mwana wa Ana anali

Disoni.

Ana a Disoni anali awa:

Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani

Ana aamuna a Ezeri anali awa:

Bilihani, Zaavani ndi Yaakani.

Ana aamuna a Disani anali awa:

Uzi ndi Arani.

Mafumu a ku Edomu

Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:

Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba.

Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.

Yobabu atamwalira, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa ufumu mʼmalo mwake.

Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.

Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka analowa ufumu mʼmalo mwake.

Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje analowa ufumu mʼmalo mwake.

Sauli atamwalira, Baala-Hanani mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.

Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. Hadadi anamwaliranso.

Mafumu a ku Edomu anali:

Timna, Aliva, Yeteti, Oholibama, Ela, Pinoni, Kenazi, Temani, Mibezari, Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu.

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero. Copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Licensed under CC BY-SA 4.0.   “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Source: eBible.org. Typeset from the source files; no intended changes to scripture wording. BibleKenya is not endorsed by the rights holder.

Full source notice & licence · CC BY-SA 4.0 · SourceEdition imported 2026-10-25.

BibleKenya

Reader settings

Theme
Font
Alignment
Reading width

Saved in this browser and used offline too. Press ? for keyboard shortcuts.